Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 13
Ngale
kodi dokotalayo akanachita bwanji zimenezi atayitanidwa kuti akathan-
dize anthu olemekezeka komanso ochita bwino, omwe ankakhala
m’nyumba zapamwamba za m’tawuni?
“Sangayerekeze kudzaponda kuno,” anatero wina panja paja.
“Akabwera mundikolowole diso limodzili.”
“Dokotala sangalole kubwera kuno Juana,” anatero Kino.
Juana ankangomuyang’ana mwamuna wakeyo modandawula. Co-
yotito anali mwana woyamba wa Juana, chipumi chokhacho chomwe
akanasiya padzikoli ngati akanamwalira. Choncho Coyotito anali
wofunika kwambiri kwa iye. Kino atawona kuti mkazi wakeyo sa-
kucheza, Nyimbo ya Banja Lake inayamba kumveka m’mutu mwake.
“Ngati sangabwere kuno, ifeyo ndi amene titamulondole,” anatero
Juana kwinaku akuponyera Coyotito kumbuyo. Kenako anamubereka
chitonga pogwiritsa ntchito shawelo yake ija ndipo anthu omwe anali
pakhomo anapereka njira kwa Juana kuti atuluke. Kino anayamba ku-
mutsatira pambuyo. Iwo anatuluka panja n’kutenga njira yolowera
m’tawuni ndipo anthu ena onse anayamba kuwatsatira. Nawonso an-
kapita nawo kwa dokotala.
Nkhaniyi inasanduka yamudzi wonse. Onse pamodzi anayenda
ngati dzombe mpaka m’tawuni. Kino ndi Juana ndi amene anali
patsogolo. Pambuyo pawo panali Juan Tomas ndi Apolonia, ndipo
chitsinda cha anthu a m’mudzi chija limodzi ndi mbumba zawo anka-
bwera kumbuyo. Dzuwa linali litakwera moti linkaponyera zinthunz-
ithunzi zawo patsogolo. Akamayenda, anthuwo ankangokhala ngati
akutsatira zinthunzithunzizo kuti aziponde.
Posakhalitsa anayamba kupeza nyumba zapamwamba zokhala ndi
mipanda yamiyala. Mkati mwa mipandayi munali maluwa okongola
ndipo m’mbali mwake munadzalidwa maluwa oyera komanso ofiyira.
Posakhalitsa gululi linadutsa mashopu mpaka linakafika patchalitchi. Pa
nthawiyi n’kuti gululi litakula kwambiri moti ena ankadabwa kuti kwa-
gwanji. Aliyense ankangokamba za Coyotito komanso zoti Kino ndi
mkazi wake akutengera mwana wawoyo kwa dokotala.
Opemphapempha omwe anali patsogolo pa tchalitchi chija anawona
7