Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 90
Miyambi ya Patsokwe
Kudzinga ngati Mtiri, tionera Mende kutha.
-Mtiri ndi mtundu wina wa mbewa ndipo mbewayi imakhala
yofatsa. Kufatsa kumawombola. Osamapupuluma ngati mende
wothawa moto, yemwe amaonedwa ndi osaka mbewa
n’kuphedwa. Tizikhazikika kuti tione m’mene zithu zithere.
Kudziwa kukoma kwa nyama n’kulinga utaidya.
-Kuti munthu anene kuti chinthu ichi n’chabwino, amayenera
kuyamba wakhala nacho.
Kudziwa mphafa ya Buluzi n’kung’amba.
-Ngati ukufuna kudziwa bwino nkhani inayake, umayenera
kufunsa komanso kukhala wodekha.
Kudziwana n’kutherana thumba lamchere.
-Kuti udziwane ndi munthu umayenera kukhala naye kwa
nthawi yaitali komanso kuchita naye zinthu zambiri.
Kudziwika sikufanana ndi kukongola.
-Si nthawi zonse pamene munthu angapeze mwayi chifukwa
cha maonekedwe abwino koma makamaka chifukwa cha khalid-
we labwino.
Kudzudzulana kumamanga mudzi.
-Kulankhulana momasuka kumathandiza kuti zinthu ziyende
bwino pamalo.
Kufa n’komwe, Tambala alira.
-Ngakhale titamwalira sikuti tambala angasiye kulira. Mwam-
biwu umatanthauza kuti tikalakwa, ngakhale tidzikometse kwa
anthu, chilango chimakhalapobe. Komanso sikuti zinthu zin-
gaime padzikoli ifeyo titamwalira.
Kufula sundwe (khwimbi) ndi nzeru.
-Sundwe ndi chakudya chakalekale. Kuti munthu atulutse
chakudya chakele ndiye kuti anasunga penapake. Choncho,
89