Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 87
Miyambi ya Patsokwe
Kuchenjera n’kosadya nako zabwino.
-Munthu wochenjeretsa anzake amadzakhala pamavuto aakulu
anzakewo akasiya kuchita naye zinthu.
Kucheza sikudzala mtanga (dengu).
-Kucheza kuyenera kukhala ndi malire n’cholinga choti tigwire
ntchito.
Kuchilendo, tema mbamu zofanana ndi eni nyumba.
-Ukakhala kuchilendo umafunika kumachita zimene eni ake
akuchita.
Kuchiza nthenda n’kuyambiza.
-Kuyambiza n’kuchita zinthu moyambirira. Kuti munthu athane
ndi matenda, amafunika kuwatulukira akangoyamba kumene.
Akakula amavuta kutuluka m’thupi. Komanso angathanthauze
kuti, kuti mwana akhale ndi khalidwe labwino umayenera ku-
mugwira dzanja n’kumamutsogolera, akalakwa osalephera ku-
mupatsa chilango kuti awongoke.
Kuchoka m’chiwaya n’kugwera pamoto.
-Mawuwa amatanthauza kuchoka pa vuto lina n’kulowa
m’mavuto ena aakulu kwambiri.
Kuchoka muukonda n’kuleza.
-Ukakhala pamavuto si bwino kumakokanso mavuto ena po-
yamba kuyankhula zambirimbiri. Ndi bwino kumadekha kuti
uchoke muukonde wa mavuto akupanikizawo.
Kuchotsa mbola n’kuzula.
-Kuti munthu achoke m’mavuto, ayenera kusiya chinthu kapena
khalidwe limene lamuika m’mavutolo.
Kuchulukana n’kwabwino, kumaipira kutha msuzi m’mbale.
-Kuchulukana n’kwabwino, kumangoipira kuti zinthu siz-
ichedwa kutha. Koma pakakhala ntchito imayenda ndithu.
86