Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 64
Miyambi ya Patsokwe
komanso kumasonyeza kukhwima maganizo. Kungoima uka-
mayankhula ndi akuluakulu ndi mwano komanso kuperewera
nzeru.
Gwira bango, ungapite ndi madzi.
-Pamavuto umachita zinthu zomwe zingakuthandize kuti upu-
lumuke.
Gwira mpini, kwacha!
-Mawuwa amanenedwa akamachenjeza munthu waulesi kuti
ayambe kugwira ntchito.
Gwira pali moyo.
-Munthu amayenera kuteteza moyo wake posamalira zinthu
zimene zimamuthandiza, monga ntchito kapena katundu.
Gwirize n’kodze.
-Munthu woyang’anira katundu wa ena ndi gwirize n’kodze
moti sakhala ndi ulamuliro pa katunduyo.
63