Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 58
Miyambi ya Patsokwe
Fodya amakoma ngwamnzako.
-Mawuwa amatanthauza kuti chinthu chanzako n’chimene
chimaoneka chokoma kuposa chako.
Fodya m’panazale.
-Ana amatengera zimene makolo awo amachita.
Fodya n’kukhomo.
-Munthu wina akapeza mnzake ali mnyumba mwake ndi mkazi
wa mnyumbamo. Pomufunsa kuti “Ukutani m’nyumba mwan-
gamo?” amati, “Ndikupempha fodya.” Mwini wakeyo amati:
“Nanga kupempha fodya amachita kulowera m’nyumba.”
Mwambiwu umatanthauza kuti tizichita zinthu modzilemekeza
kuti tisasokoneza maganizo a anthu ena.
Fodya wako ndi uyo ali pamphuno, wapachala ngwa mphepo.
-Munthu ayenera kumakhutitsidwa ndi zomwe ali nazo, chifu-
kwa zimene amafuna kapena amamva akhoza osadzazipeza
pamoyo wake.
Fodya wako ndi uyo ali pamphuno.
-Tizidalira zinthu zomwe tili nazo kusiyana ndi zomwe
tikungoganizira.
Fulukutufulukutu kuti anzake kumudzi aziti akulima.
-Sibwino kumangodzitama kapenanso kumachita zinthu
modzionetsera. Ndi bwino kumagwira ntchito zooneka ndi
maso m’malo momangodzitama. Ndi bwino kumachita zimene
umanena.
Fupa lokakamiza limagulula dzino.
-Zinthu zokakamiza sizichedwa kutha ndipo nthawi zina zimao-
nonga zinthu zina.
57