Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 53
Miyambi ya Patsokwe
Dzenje la pida (pinji) limadziwika n’kuunjika.
-Anthu akamapanda kukuyankhula kapena kumangokhala ndi
msunamo umadziwa kuti pali nkhani.
Dzera uko sikuyenda, koma tiye kuno.
-Pophunzitsa ena ntchito kapena zinazake, si bwino kungofotok-
oza chabe, tizionetsa chitsanzo chabwino kuti malangizo athu
akhale aphindu.
Dziko la eni ndi mowa, ukaponda waledzera.
-Munthu ukayenda umayenera kukumbukira kuti ndiwe mlen-
do. Ukalakwitsa zabwino zako zonse zimaiwalika.
Dziko lingagwe.
-Ukasiya ntchito yomwe munthu umagwira n’kuyamba ina
ndiye munthu n’kumakufunsa: “Bwanji mutsirize kaye ntchito
yomwe munayamba kaleyi?” Kuyankha kwake mokana umati:
“Dziko lingagwe.”
Dziko ndi mafuwa, achita kuchilikizana.
-Munthu aliyense ali ndi mbali yake kuti zinthu ziyende bwino
m’dziko kapena m’mudzi.
Dziko ndi anthu, nyama ndi mambala.
-Anthu ndi amene amakometsa dziko. Choncho, pafunika kuti
anthu azigwirizana kuti zinthu ziziyenda bwino pamudzi pawo.
Asamangokhala ngati nyama zomwe zimadyana zokhazokha.
Dziko ndi mafuwa achita kuchinjiriza.
-Kuti dziko liyende bwino pamafunika anthu ena oliteteza, ena
odziwa zamalamulo ndiponso ena olamulira. Osangoti mfumu
imodzi yokha ayi. Ngati zitakhala choncho mtendere sungakha-
lepo.
Dziko ndi wanu, ndalama ndi wathu.
-Mawuwa amatanthauza kuti tinabwera kuno kudzapanga
52