Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 42
Miyambi ya Patsokwe
ndi anthu basi. Choncho, tifunika kumawasamalira komanso ku-
wapirira.
Chingwe ndicho chithera msampha mphamvu.
-Tikamangomvera nkhani zabodza za anthu ena tingadziputire
mlandu. Zikhoza kutitsatira n’kupeza nazo mavuto.
Chingwinjiri maliralira, chinalira m’msolo wa mbala.
-Munthu ukakhala wapakamwa, umadzanena zinthu zina kwa
ena omwe amafuna kudziwa zimenezo ndipo umapeza mavuto.
Chinsanjesanje chinaoletsa mazira a mpheta.
-Munthu wansanje amachedwa ndi kufufuza mkazi kapena
mwamuna wake, potero amadziwitsa ena za khalidwe la
mwamuna kapena mkazi wakeyo n’kudziwonongera banja.
Chinsisi sichikhala pa anthu awiri.
-Ukauza mnzako nkhani yachinsisi n’kumukhulupirira, uma-
khala ukudzinamiza chifukwa nayenso amakhala ndi anzake
ena apamtima.
Chinthu chikataika chimalira mwini wake, monganso mwini
wake ali kuchilira.
-Ngati tatola chinthu chamwini tiyenera kuchibweza kuopera
kuti chingatisowetse mtendere mumtima popeza timaoneka
ngati tachiba.
Chinthu ndi mtima, kanthu ndi khama.
-Pamene waikapo mtima wako, uyenera kuchita khama kuti
chinthucho chitheke.
Chinziri chimanyang’wa ndi tsala lake (lakwawo).
-Munthu aliyense amanyadira zinthu zake monga zovala, ntchi-
to ndiponso banja lake.
Chipande cha therere chimakoma n’kuyenderana.
-Kuti mnzako akuchitire zabwino pafunika kumubwezera
41