Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 271
Miyambi ya Patsokwe
Zipupa zili ndi makutu.
-Tizionetsetsa tisananena zachinsinsi chifukwa makutu ali
ponseponse.
Zizikanika zitayang’anana.
-Ndi bwino kumayesetsa kuchita khama pochita zinthu. Zichite
kukanika zokha.
Zizingokomera mbuzi kugunda galu, galu akati alumeko akuti
waboola nguwo.
-Munthu wokondedwa kapena wotchuka akachitira ena zoipa,
si kawirikawiri kumudzudzula. Koma munthu wooneka ngati
wopanda ntchito akachitira anthu ngati amenewa zoipa ama-
landira chilango chokhwima.
Zokoma zili m’tsogolo.
-Munthu ukachita khama umadzakhala pabwino.
Zolowere n’kudyere mwana.
-Mawuwa amanenedwa pochenjeza munthu kuti akufuna aku-
chitire zoipa pokunyengerera.
Zonse ndi moyo.
-Kuti munthu achite chilichonse amafunika kukhala ndi moyo.
Munthu ngati ali moyo akhoza kuchita chilichonse chimene aku-
funa.
Zonse ndi nthawi.
-Chilichonse chimachitika pa nthawi yake.
Zumba likoma ndi nsinjiro.
-Nkhani yongomva imapita iwonjerezeredwa mpaka
imasokoneza zinthu. Zumba ndi masamba owawa. Amakonda
ndi nsinjiro.
270