Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 269
Miyambi ya Patsokwe
Zawombera mpeni.
-Zomwe ndimafuna zalephereka, ndalephera.
Zembeni kumowa, kumlandu andiitana.
-Anthu ena amaitana anzawo zikavuta, zikamayenda amawa-
taya.
Zengerezu adalinda kwawukwawu.
-Kuzengereza kumagwetsera munthu m’mavuto. Kungatileph-
eretsenso kuchita zinthu zofunika kwambiri.
Zidze pano n’za tonse.
-Pamudzi pakagwa mavuto timayenera kuthandizana.
Zigwinjiri maliralira, zinalira mumsongolo wa mbala.
-Munthu wina ataba zingwinjiri anagwidwa zitalira m’thumba.
Choipa sichingabisike chimaululika.
Zika ukaona, Kamba anga mwala.
-Kamba ngati sakusuntha amaoneka ngati mwala. Nkhani zina
zimakhala zosamvetsetseka. Wina akhoza kudwala mwakayaka-
ya, koma wina wolimba n’kumwalira kusiya wodwalayo.
Zikachuluka sizidyeka.
-Ndi bwino kumachita chinthu chimodzi pa nthawi imodzi.
Zikagwera pamphuno sizidyeka.
-Mawuwa amanena za munthu amene akulephera kugamula
mlandu chifukwa choti ndi wa m’bale wake.
Zikatalika zala ngati nkhonje wakhobwe.
-Mawuwa amanena za munthu wakuba.
Zikungokhala pachilowelo.
-Mwambiwu umanena za anthu amene akubwera ku-
madzapempha chifukwa choti amva zoti anzawo anapatsidwa.
Mwachitsanzo, mwana akakhala m’chilowero anthu amabwera
268