Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 266
Miyambi ya Patsokwe
Yagwa m’mbale ndi ndiwo.
-Tisamasankhe ndiwo tikamadya.
Yakondwa nkhwichi, Kalulu wakwiya.
-Anthu ena sakondwa mnzawo akatukuka.
Yangeyange adaphetsa kangaude.
-Tiyenera kumachita zinthu mwadongosolo komanso mogwiri-
zana kuti tisapeze mavuto.
Yaphwa nyanja ana atole nkhombe.
-Mauwa amanena za mavuto amene ana amakumana nawo
chifukwa choti makolo awo amwalira.
Yaponda thope yamwa.
-Pakakhala chizindikiro chinachake ndiye kuti chinthucho
chachitikadi.
Yemwe umam’konda usamubwereke ndalama.
-Munthu amene umamukonda akhoza kukukhumudwitsa ngati
utamubwereka ndalama iyeyo osabweza. Posonyeza kumukon-
da, popeza ambiri sabweza ngongole, ndi bwino usamubwereke.
Yotema ndi nkhwangwa udzadya, ya mpeni sudzadya.
-Munthu akatema nyama ndi nkhwangwa anthu ena amamva
ndipo amabwera kuti adzadye nawo. Koma yodula ndi mpeni
palibe amadziwa. Tisamachite zinthu modzionetsera.
265