Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 261
Miyambi ya Patsokwe
Wolirira kwawo adapita ndi madzi.
-Mawuwa amachenjeza munthu amene akuchita makani anzake
akamamulangiza. Anthu ngati amenewa amakhala ngati akudzi-
wa zonse ndipo pamapeto pake amakumana ndi mavuto oopsa.
Wolondera chitsime safa ndi ludzu.
-Munthu amadyera ntchito imene amagwira monga wodikirira
chitsime sangasowe madzi.
Woluka nsengwa (malichero) adyera m’chipapa.
-Nthawi zina munthu wogwira ntchito zaluso sakonda
kutengako chimodzi chifukwa choganiza kuti akatero akuwo-
nonga. Iye amagwiritsa ntchito zipangizo zakutha kapena
zosweka.
Wongolozera kumtondo, kumunda kulibe ndime.
-Mawuwa amanena kuti tisamakhale aulesi, anthu omangokon-
da kudya osati kulima.
Wonukha samadzimva, amamumva ndi anzake.
-N’zovuta munthu kudziwa kulakwa kwako kapena makhalid-
we ako oipa koma anzako. Ndi bwino kumafunsako ena kuti ati-
uze mavuto athu.
Wopempha salira tololo.
-Tizikhutitsidwa ndi zomwe tili nazo kapena tapatsidwa.
Mwachitsanzo, munthu wopemphetsa samafuna kuti amupatse
zodzadza thumba.
Wopemphetsa sakulitsa chitete.
-Wopemphetsa amafunika kumakhutira ndi zimene wapatsid-
wa.
Wophikira ena amafa ndi njala.
-Tiziyamba kuona zosowa zathu kaye tisanayambe kuthandiza
ena.
260