Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 252
Miyambi ya Patsokwe
Wakufa sadziwika.
-Mawuwa amanenedwa anthu akamakangana n’kumanena kuti
ndili ndi mphamvu kwambiri ndine. Nkhani yake imanena kuti,
panali nkhanga ndi finye ndipo tsiku lina zonse zikuyenda zi-
nakumana. Nkhanga inati: “Ndimakufuna iwe! Wafa lero! Koma
finye anangoti: “Wakufa sadziwika!” Nkhanga inati, “Iwe ndi
mwana wamwano eti? Ine ndikuti wafa lero!” Mmeneno n’kuti
nkhanga itayamba kale kujompha finye, uku finye akutulutsa
utomoni woyera womwe unali kukakamira pamlomo wa nkhan-
gayo. Nkhanga inayamba kulephera kupuma ndipo inafa.
Wogonja kapena wakufa sadziwika mpaka zonse zitafika
pamapeto pake.
Wakumba cha nje! mtengo wausiya.
-Mawuwa amanenedwa ngati munthu walephera kupeza
zimene amafuna kapena walephera kudziwa zoona zenizeni.
Wakutsina khutu ndi mnansi.
-Amene amakuchenjeza amakhala m’bale wako komanso ama-
sonyeza kuti amakuganizira.
Wakwatira kwa mphezi, saopa kung’anima.
-Munthu amene akufunitsitsa chinthu ayenera kukhala wolimba
mtima. Chilichonse chili ndi zovuta zake choncho si bwino
kungosiya kuchita zinthuzo chifukwa choti ukukumana ndi
mavuto. Ukamayamba kuchita zinthu umayenera kuganizira
mavuto ake.
Wakwatira mende, waleka chitute.
-Mende samsunga chakudya anthu akangokolola, pomwe chi-
tute amasunga. Ndiye munthu m’malo mokwara ndi mende
wosunga chakudya, wakwatira mlesi weniweni chitute chifukwa
cha kukongola. Tikamachita zinthu tizionetsetsa kuti tikusankha
251