Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 241
Miyambi ya Patsokwe
Umachokera pamodzi ndi mawu.
-Munthu akanena kanthu umayenera kuchita zomwezo osati zi-
na.
Umadikira kuti mafulufute atuluke.
-Si bwino kumachita phuma pochita zinthu chifukwa zimenezo
zingachititse kuti titaye mwayi kapena titsekezereze zabwino.
Umaingitsa kachoka, walinga iwe nutola.
-Munthu amene wakumana ndi zambiri ndi amene amayank-
hula zogwira mtima. Munthu amene anali ndi khalidwe
loipitsitsa ndi amene amaphunzitsa bwino.
Umakongola ukusangalala, koma umabweza ukulira.
-Ngongole imakoma ukamabwereka. Tizisamala ndi nkhani
yobwereka ndalama.
Umakumbukira mwana akapsa.
-Kawirikawiri sitichenjeza anzathu mpaka atalowa m’mavuto.
Umalawa zogagada ndi nkhwangwa, zocheka ndi mpeni suzi-
lawa.
-Tisamalakelake kukhala ndi zinthu zapamwamba kwambiri
n’kumanyoza zing’onozing’ono.
Umanena chatsitsa dzaye kuti Njovu ithyoke mnyanga.
-Tizinena chayambitsa nkhani yeniyeni. Anthu ena ankadabwa
kuti n’chiyani chathyola mnyanga wa Njovu. Atafufuza bwinob-
wino anapeza kuti mumtengo wa maye munali nyani. Nyaniyo
ndi amene anagwetsa dzaye kuti Njovu ithyoke mnyanga.
Umanjata thumba tokoma tikuuluka.
-Ena amabisa zoipa, koma akamamanga thumba lawo la zoipazo
zina zimauluka n’kudziwika kwa aliyense.
240