Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 232
Miyambi ya Patsokwe
Ukalemera, abale sakondwera.
-Zinthu zikamakuyendera kapena ukakhala pabwino, anthu
sasangalala. Amafuna kuti chinachake choipa chimuchitikire
kuti mufanane.
Ukalira mzinda usamapse mtima.
-Ngati mfumu ikufuna kukhala ndi mudzi waukulu, iyenera
kupewa kupsa mtima. Mtsogoleri amafunika kukhala woleza
mtima.
Ukamachoka umachoka bwino, suchoka utakhadzula mnzako
mlomo.
-Mlendo amayenera kuchoka bwino pamalo, apo ayi anthu san-
gadzamulandirenso. Anthu sangalandire munthu amene
wachoka pakhomo atakhadzula mlomo wa mnzake.
Ukamafuna dzino lalitali, uzikhala ndi mlomo wovindikirira
dzinolo.
-Ukamawaputa mavuto kumadziwa kuti uthana nawo bwanji.
Osamayamba kuchita chinthu ulibe mapulani.
Ukanama sikuchedwa kucha.
-Ukanena zabodza suchedwa kugwidwa. Chitsanzo: Ngati
utanamiza wangongole kuti abwere mawa, sikumachidwa
kucha.
Ukaona chalero, usataye chakale.
-Ndi bwino kumasunga zinthu zakale, osazitaya chifukwa choti
tapeza zina.
Ukaona mtanda kukula ndiye umati, “ndim’lere mwana
wanuyu!”
-Anthu ena amakonda kapena kuchitira zabwino anzawo
akaona kuti apindulapo kenakake. Mwachitsanzo, kuuza mun-
thu kuti amulelera mwana chonsecho akufuna amunyengerere
231