Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 22
Miyambi ya Patsokwe
Chabadwa chafa, chili kumpani chauma.
-Ngati munthu uli ndi moyo, dziwa kuti udzafa ndithu ndipon-
so mavuto udzakumana nawo.
Chadodometsa mleme chili ndi khambi.
-Munthu akasiya chizolowezi chake ndiye kuti chilipo chimene
chamudabwitsa kapena chamuchititsa mantha. Ukaona chomwe
wina chamupezetsa tsoka, umayesetsa kupewa kuchita zomwe-
zo.
Chadza ndi yani chokwera ndi mwana kunkhokwe?
-Tisamachite zomwe zingabweretsere ena mavuto. Kale anthu
ankapewa kukwera ndi mwana munkhokwe kuopa kugwa ndi
mwanayo n’kumuvulaza.
Chadza ndi yani chopha nkhuku anzanu akudwala dzino?
-Mawuwa amanenedwa munthu akachita zinazake zomwe
akudziwiratu kuti nzake sachita nawo chifukwa akudwala
kapena wapanikizika ndi zina.
Chafa chaola, phwiti wasekera nthenga.
-Munthu akamwalira, si anthu onse omwe amaliradi chifukwa
cha chisoni. Ena amalira kwinaku akusangalala kuti adzatenge
chuma chamasiye kapena adzalowe udindo wa womwalirayo.
Chafuna mwini chili kwa Bongololo (kwa Mandala).
-Munthu ukafunitsitsa chinthu, ndi bwino kulimbikira kugwira
ntchito ndipo ukhoza kuchipeza.
Chagwa pamtutu sichidyeka.
-Mwambiwu umanena za munthu amene akulephera kugamula
mlandu chifukwa mlanduwo ndi wa m’bale wake.
Chagwera pamfuno sichidyeka.
-Mwambiwu umanena za munthu amene akulephera kugamula
mlandu chifukwa mlanduwo ndi wa m’bale wake.
21