Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 219

Miyambi ya Patsokwe amene angamasule ndi tambwali mnzake. Tidauluka tidapangana, mavu adaning’a onse. -Anthu amafunika kupangana kuti zinthu ziyende monga pami- landu ndi zina. Tikapha Mwiri m’mphako, koma kuloza mwendo momwemo kuti tiphe wina. -Tikapeza mwayi, tisasiyire pomwepo, tipitirizebe mpaka titape- za wina. Tikhale nawo adalanda malo. -Pali anthu ena omwe amabwera pamudzi kuti adzapemphe ma- lo, koma kenako amalanda malo kapena kuyamba kulamulira. Timba anathyola mwendo dansi yothaitha. -Munthu akamachita zinthu mopitirira muyezo amakumana ndi mavuto. Ndi bwino kumasamala ndi zinthu zikakhala ku- mapeto, umatha kukumana ndi mavuto. Timba sachepa ndi mazira ake. -Tisamanyoze munthu chifukwa cha zimene ali nazo. Munthu sachepa ndi zinthu zake. Tinamva kale zanu. -Palibe chinthu chatsopano chomwe mungatiuze. Tinthu m’nkhuni adalekera mwana wa mkazi mnzake ku njoka. -Tikamva zoti penapake pali zovuta tiyenera kupitapo tokha m’malo mouza wina kuti apite, chifukwa tingamuphetse. Zili ngati kutumiza mwana kuti akaone chomwe chili pamtolo n’kukamulumitsa njoka. Tizisinja kamba, kuyenda kwa ulendo sikudziwika. -Kamba ndi chakudya cha paulendo. Ndi bwino kumakonzekera zapatsogolo kuti tisapeze mavuto monga kukonzeratu chakudya 218