Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 208
Miyambi ya Patsokwe
Pamene pali ntchito pamakhalanso mavuto.
Patsala paja pagona chinziri.
-Nthawi zina ngakhale mlandu uweruzidwe, anthu amasungi-
ranabe chakukhosi, enanso amadandaula kuti mlanduwo
sunagamulidwe bwino. Amakhala ngati akunena kuti “patsala
paja pagona chinziri.”
Patse salira tololo.
-Munthu wopemphetsa amafunika kungolandira zimene wap-
atsidwazo. Mphatso simadzadza dengu.
Patsogolo mpambuyo pomwe.
-Nthawi zina amene ali patsogolo amatha kukhala pambuyo
ngati anthuwo atauzidwa kuti atembunuke. Chimodzimodzi ndi
mwayi umene ena ali nawo, mawa zikhoza kutembenuka
n’kupezeka kuti ndi wathu.
Paunjikana mtchembere pali bodza.
-Azimayi akakhala pagulu nthawi zambiri amakonda kukamba
mabodza.
Paunjinji samabuulirapo.
-Tisamayankhule pagulu zinthu zachinsinsi monga nkhani za
m’banja ndi zina chifukwa zikhoza kungoyalutsa ife tomwe.
Paunjinji savulirapo.
-Nkhani zina zachinsinsi sitimaulula pagulu poopa kupusa.
Paunyinji sabubulirapo.
-Anthu ena omwe safuna kuti anzawo amveko zachinsinsi zawo
amayesetsa kuti akambirane zachinsinsizo enawo akachokapo
kapena amapita pamalo oduka mphepo.
Pavinidwa mfulu, kapolo amavinidwa pomwepo.
-Munthu amadyerera akakhala kuti amakhala bwino ndi anzake
ochita bwino.
207