Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 206
Miyambi ya Patsokwe
Pamudzi pakakhala pa zitsiru mkamwini asamakulirepo
phazi.
-Ukakhala pamudzi wa eni usamadzionetse kuti ndiwe wanzeru
chifukwa sungadziwe zomwe eni mudzi amapangana.
Pamudzi pamakoma ndi ana.
-Pakhomo popanda ana sipasangalatsa.
Pamudzi podziwadziwa, koma akusochera.
-Mawuwa amanena za munthu amene akulephera kuchita chin-
thu chimene akuchidziwa, ngati yemwe akusochera m’mudzi
womwe wakulira.
Pang’onopang’ono ndi mtolo.
-Zinthu zikuluzikulu zimayamba ndi zinthu zing’onozing’ono.
Mwambiwu umatiphunzitsanso kuti kuchita zinthu
mwachifatse n’kothandiza kusiyana n’kuchita zinthu mopupu-
luma.
Panga chosankha utakwiya kuti kenako unong’oneze bondo.
-Ukamachita zinthu kapena kumasankha zinthu utakwiya,
umapezeka kuti wasankha kapena kuchita zinthu zolakwika
n’kumadziimba mlandu pambuyo pake.
Pankhondo sasekana.
-Chibwana sichimafunika pantchito pa zinthu zofunika monga
nkhondo.
Pantchito mpachikamwini, amakuchotsa ndi usiku.
-Ndi bwino kumakonzeratu zimene ungachite utachotsedwa
ntchito chifukwa sudziwa kuti ndi liti pamene udzachoke. Ku-
masamalira ntchito pogwira ntchitoyo molimbika.
Pantchito n’kudyerana.
-Anthu omwe amagwira ntchito limodzi amakonda kuchitira
205