Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 202
Miyambi ya Patsokwe
chochita.”
Pafera kambuku pali matatalazi.
-Pamene pagonja wamphamvu kwambiri pali mavuto.
Pafera munthu salephera kudzumapo.
-Munthu mavuto akamupanikiza amadzuma ndipo ena amamva
n’kumuthandiza.
Pafuka utsi pali moto.
-Mphekesera iliyonse imakhala ndi nkhanikhani.
Pafupi ndi apo wafika.
-Osamadalira zinthu zomwe sunapeze. Ndi bwino kumathokoza
zimene uli nazo.
Pafupi padaolera njovu.
-Njovu itafa anthu ankati ili pafupi koma kuli kutali moti mpaka
njovuyo inaola anthu asanapiteko. Ukamafuna kugwira ntchito,
ngakhale yaing’ono, umafunika kukonzekera bwino kuti uimal-
ize m’malo momangoiderera.
Pagona tonde padzinunkha.
-Munthu aliyense ayenera kuchita khama pantchito kuti
padzioneka kuti panali munthu.
Pagule fumbi ndiwe mwini.
-Munthu aliyense amalimbikira kuchita zinthu zake. Amaonet-
setsa kuti zachitika bwino kwambiri koposa mmene akanachitira
za ena.
Pagwa fisi paterera.
-Pamene munthu wamkulu walakwa ndiye kuti panavuta.
Pakadafunda padajiwitsa galu.
-Tsiku lina galu anagona penapake pamene pamkamveka bee,
moti mpaka analephera kukalowa m’nyumba ndipo anagona
pomwepo. Fisi atabwera anangomutola. Kukakamira kuchita
201