Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 200

Miyambi ya Patsokwe Osatsinira mafulufute kuuna. -Munthu ukapeza mwayi winawake, uyenera kupewa kuchita zinthu zomwe zingatsekereze mwayiwo. Osaotcha mlatho umene waolokera, ungadzaufune ukamabw- erera. -Usamanyoza kapena kuwononga zinthu zonse zatithandiza. Oyanjana sagona nyumba imodzi. -Mpofunika kumakondananso ndi anthu ena m’malo mon- gokonda munthu m’modzi. Oyenga mafuta satuwa. -Anthu amene amachita zinazake amakhala oyambirira kupin- dula ndi zinthuzo. 199