Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 2
Miyambi ya Patsokwe
Miyambi ya Patsokwe
Miyambi, kapena ku ti mikuluwiko, ndi m aw u okhala
ndi tanthauzo lobisika kapena lophiphiritsa. Nthawi zambiri
imakhala chiganizo, ndipo kawirikawiri imakhala mutu wa
nkhani kapena nthano inayake. Munthu akaponya mwambi, an-
thu amakumbukira nkhani yake yonse komanso phunziro lake.
Miyambi ndi chida chabwino kwambiri pothandiza ena. Ukhoza
kupereka malangizo amphamvu, kudzudzula kapena kuchenjeza
munthu popanda kumukhumudwitsa. Ena amanena miyambi
pofuna kubisa tanthauzo la zomwe akunena kuti ana a makutu
akuthwa kapena anthu ena asadziwe zimene akutanthauza.
Timaponyanso miyambi pofuna kukometsera nkhani kuti isa-
khale yozizira, koma kuti ikhale ndi chikoka. Kungoti pamafu-
nika ukadaulo kuti tiluke nkhani n’kuponya mikuluwikoyo pa-
malo oyenera. N’chifukwa chake kudziwa tanthauzo la mwambi
ulionse n’kofunika kwambiri.
The Series Of Rodgers Bounty Books [RBB]
Copyright © January 2016 by Bonwell “Kadyankena” Rodgers.
All rights reserved. No part of this publication may be reproduced or transmitted in any form or by any means,
electronical or mechanical, including photocopy, recording or any imformation storage and retrieval system,
without permission in writing from the owner.
Requests for permission should be mailed to: [email protected]
Phone: 0881813953, 0881831435
1