Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 189

Miyambi ya Patsokwe Nkhuyu zodya mwana zidapota akulu. -Nthawi zambiri ana akapalamula vuto lonse limafikira kwa ma- kolo ndipo makolowo ndi amene amavutika nalo. Nkhwangwa ikati chubwi m’madzi, dzanja lako lipite pom- wepo. -Tisamazengereze kuchita zinthu. Mavuto kapena zina zikachi- tika, ndi bwino kuchitiratu chifukwa tikachita ulesi zikhoza kutisokonekera. Nkhwangwa imakhulupirira mpini. -Anthu amayenera kukhulupirirana komanso kuthandzana kuti zinthu ziyende. Nkhwangwa siithwera pachipala. -Munthu samaphunzira zonse kusukulu, kuchinamwali kapena kwa makolo ake. Amatha kuphunzira zina akamachita zinthu ndi anthu ena. Nkhwangwa yatema bondo. -Nkhwangwa yako ikakutema sumaiwala. M’bale wako akaku- lakwira ndi bwino kumukhululukira m’malo momangosunga chakukhosi. Nkhwangwa yobwereka siichedwa kuguluka. -Munthu sachedwa kuchita ngozi ndi chinthu chobwereka. Nkhwangwa yobwereka sichedwa kusweka mpini. -Munthu sachedwa kuchita ngozi ndi chinthu chobwereka. Nkhwangwa yobwereka siichedwa kuthyoka. -Zinthu zobwereka sizikhalitsa, umafunika kupeza zako. Nkhwani saotchera. -Mawuwa anganenedwe ngati wina wachita zinthu zabwino kwambiri moti sitingachitirenso mwina koma kumuyamikira. Anganenedwenso ngati wina akuyesa kuchita zosatheka. 188