Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 179

Miyambi ya Patsokwe Ndam’meta mpala wopanda madzi. -Munthu amanena mawuwa potanthauza kuti wamuchenjeretsa winawake kapena wamukhaulitsa. Ndangotsala madzi amodzi. -Mawuwa amatanthauza kuti ndangotsala pang’ono kufa. Ndani amene angaike khala lamoto pamalaya ake koma osapsa? -Palibe munthu amene angachite choipa osakumana ndi zotsati- ra zake. Ndapakonda adasiya khonde. -Kuzengereza pochita zinthu kumapezetsa mavuto. Ndaphwa mafuta, patsala thonje lokha. -Mawuwa amatanthauza kuti munthu ali ndi njala. Kuphwa ma- futa akutanthauza kuti wapuma koma akumva njala. Ndawonera momwemu mwambi wa gulugufe. -Ndi bwino kumakhutitsidwa ndi zimene uli nazo ngakhale zili zochepa. Ndayala mayani, awuma. -Ndadikira mokwanira moti ndatopa. Ndewonetsetse adathetsa nkhosa. -Kuzengereza kumagwetsera munthu m’mavuto. Ndewu siimanga mudzi. -Mikangano komanso ndewu zimapasula mudzi. M’malo mo- chita zimenezi ndi bwino kukambirana mwamtendere. Ndi bwino kunena maganizo ako udakali ndi moyo, kusiyana n’kumadzawanena ukutsirizika. -Osamamangika kunena maganizo ako chifukwa mwina angathandize. 178