Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 177
Miyambi ya Patsokwe
N’takalamba n’kusiya dziko likali nsonga.
-Mawuwa amanenedwa munthu akamafuna kunena kuti akufu-
na kuchoka zinthu zikadali bwino, pamalo pasanaipe.
Nachonso chitsiru chili ndi mwini.
-Munthu ngakhale wopusa amakhala ndi m’bale wake amene
amamukonda. Akaphedwa abale ake adzaoneka. Choncho si
bwino kunyoza ena chifukwa cha khalidwe kapena maon-
ekedwe awo.
Nalikukuti saluma, koma akaluma alibe chivumulo.
-Pali anthu ena omwe amaoneka a phee, koma tsiku lina
ukadzawaputa umadzaona kuti ali ndi ululu woopsa kuposa wa
njoka.
Namkwichi akaona akazi ndiye amakondwa.
-Namkwichi ndi mbalame yokonda akazi kwambiri. Mwam-
biwu umanena za munthu wokonda akazi.
Nankholowa ali m’manja n’kulinga utalawa.
-Pali njira zosiyanasiyana zophikira nankholowa (masamba a
mbatata). Tisamaweruze nsanga chinthu tisakuchidziwa bwino.
Nankungwi chilanga anzake, mwake sazira.
-Pali anthu ena omwe amakonda kulangiza anzawo pomwe
iwowo sachita zimenezo, kapena alibiretu khalidwe.
Nankununkha sadzimva.
-N’kovuta kuti munthu adziwe za momwe anthu ena amamuon-
era makhalidwe ndi maonekedwe ake, koma anthu enawo ndi-
wo amamudziwa bwino.
Nanzeze apitira m’kuleza.
-Timanena mawu amenewa munthu akawomboka pamavuto
amene anawapeza kuchokera kwa anthu amene sanamvetse
bwino nkhani yonse. Ngati Nanzeze yemwe anapulumuka
176