Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 165
Miyambi ya Patsokwe
Munthu wopanda maso samunamiza maso.
-Tisamalonjeze zinthu zomwe sitingakwanitse kuchita, monga
kuchititsa kuti wakhungu aone.
Munthu wopata safa ndi chuma.
-Munthu akamwalira samatenga chuma kumanda. Choncho
ngakhale tilemere, si bwino kumayerekedwa chifukwa ndalama
sizingatiike m’manda.
Munthu wosabala amasowa chomutukwanira mwamuna.
-Mayi amene ali ndi mwana amatha kum’tukwana mwana wake
pamene wayambana ndi mwamuna wake. Akakhala wopanda
mwana amasowa womutukwana.
Munthu wosauka sapha nyama ya nguwo.
-Munthu umayenera kufufuza zinthu mogwirizana ndi mmene
umapezera zinthu. Osamafuna zinthu zomwe sungathe kuzipe-
za.
Munthu wotolatola samera ndevu zoyera.
-Munthu wamakhalidwe oipa sakalamba.
Musade Vumbwe, akudya nkhukhu ndi Kalulu.
-Nthawi zambiri pamudzi pakachitika zoipa amaganiza kuti
mdani wawo ndi amene wawachitira zimenezo. Koma nthawi
zina anthu omwe amaoneka ngati Akalulu ndi amene amakhala
atachita zoipazo.
Musamati ndi masweswe lili dazi.
-Si bwino kumanyozera zinthu anthu ena akamanena.
Musamati ndikuthawa mlomo, mlomo uli kulikonse.
-Kuthawa mlomo ndi kuthawa kulongolola. Mavuto ali
ponseponse ndipo sitingawathawe. Amene akufuna kuwathawa
kuli bwino angomwalira.
164