Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 160
Miyambi ya Patsokwe
kwa iwo basi, ngati mmene munthu amakwerera mumtengo
kuti akangothyola mango basi.
Mtengo wopanda tsinde mudauonapo?
-Ngati tikufuna kuona khalidwe la ana ndi bwino tiyang’ane
makolo awo. Kuti umvetse zochita za munthu wina ndi bwino
kufufuza mbiri yake.
Mthamangira kuotha anasiya moto ukuyaka.
-Munthu wothamangira kuchita zinthu ndi amene amayambiri-
ra kukumana ndi mavuto. Ndiye anzake amabwera n’kudzape-
za zabwino, apo ayi amaphunzirira pa tsoka lakelo.
Mthanga kunena adapisa Likongwe wa apongozi.
-Mwambiwu umanena za mkamwini wina yemwe anafulumira
kapena kuti kuthanga kunena kuti amene atathawitse Likongwe
asamuka pamudzi. Ndiye zinachitika kuti iyeyo ndi amene
anathawitsa Likongweyo ndipo zinamuvuta. Tisamalonjeze
msanga za chinthu chomwe sitikudziwa kuti chitha bwanji.
Mtima suvala nsanza.
-Munthu akhoza kukhala wosauka, koma mumtima mwake
n’kukhala wolemera kwambiri pa zimene amakhumba. Palibe
amalota ali wosauka.
Mtima uli ngwizi, kadziwe ka mu Likuni.
-Mwambiwu umanenedwa pofuna kutanthauza kuti wakwiya
kwambiri, uli ndi nkwiyo wosaneneka.
Mtima ulikuperewera, chanka patali.
-Ngati mtima sukhumbira chinachake ndiye kuti n’zosatheka
kuchipeza.
Mtima wabwino ngwaumulungu.
-Munthu wamtima wabwino amachitanso zabwino.
159