Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 156
Miyambi ya Patsokwe
Mphepo yakumpoto indachititsa mkamwini kuba m’munda
mwa apongozi.
-Umphawi kapena mavuto ena chisamakhale chifukwa
chochitira zoipa monga kuba, kutukwana ndi zina.
Mphini yobwereza ndi imene imawala.
-Malangizo obwereza ndi amene amamveka bwino.
Mphongo ya Chiwala sichepa.
-Si bwino kunyoza amuna kapena akazi a ena chifukwa ndi
amuna kapena akazi awo basi.
Mphongo zidana.
-Nthawi zambiri amuna sachitira amuna anzawo zabwino. Ko-
ma akakhala mkazi amatha kumuchira zabwino kwambiri.
Mphungu sataya nthenga.
-Mawuwa amanena za munthu woumira. Mphungu ndi
mbalame imene imauluka m’mwamba kwambiri, koma ikag-
wetsa nthenga, imawakha mthengayo isanafike pansi.
Mphuno imodzi silowa zala ziwiri.
-Si bwino kuchita zinthu ziwiri nthawi imodzi chifukwa nthawi
zina umatha kulephera kukwaniritsa zonsezo.
Mphuno salota, adawombera mfiti m’manja.
-Munthu woipa kapena wabwino alibe fungo. Nthawi zina ame-
ne timawaona ngati abwino ndi amene amadzatipha. Ukhoza
kuchitira zabwino munthu amene angadzakunyoze patsogolo.
Mphwanga ndiye wamkulu msinkhu, ngakhale kuti ndi-
natsogola ndine.
-Kukhala ndi mnzeru si kubadwa kale kapena kutalika.
Mphwanga, mukakula bwino ngati mwana wa Mlamba.
-Ndi bwino kumakhala wochenjera ndiponso kumakhala bwino
155