Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 154
Miyambi ya Patsokwe
Mpandamachokero, anakodzera moto wa ana.
-Kumakhala ndi chifukwa chenicheni pochoka pamalo monga
kuchikamwini kapena pantchito. Osamagwiritsa ntchito zifukwa
zosamveka.
Mpandamachokero, mkamwini anachokera mamina.
-Kumakhala ndi chifukwa chenicheni pochoka pamalo monga
kuchikamwini kapena pantchito. Osamagwiritsa ntchito zifukwa
zosamveka.
Mpani wa mbewa utsatira mwini.
-Munthu aliyense amalimbikira kuchita zinthu zake. Amaonet-
setsa kuti zachitika bwino kwambiri koposa mmene akanachitira
za ena. Ungatanthauzenso kuti choipa chimatsata mwini. Uka-
palamula, ngakhale utathawa kapena patapita nthawi yaitali
bwanji, tchimo wachitalo limakulondola, ndipo kenako limaku-
luma.
Mpatse fupa mwana atonthole.
-Nthawi zina ndi bwino kumalolera kuti ana achite zofuna
zawo. Ndi bwino kumaloleza maganizo kapena zimene anthu
ena akufuna kuti aphunzirepo kathu.
Mpatseni tione chakhalitsa galu pakhomo.
-Pamudzi pakakhala mapokoso kapena mavuto ena, timafunika
kuonetsetsa kuti tidziwe chimene chayambitsa vutolo.
Mpeni ulibe bwenzi.
-Munthu akakhala woipa sakhala ndi bwenzi ndipo anthu ama-
muopa kuti tsiku lina angadzawachitire zachipongwe. Mpeni
umatha kupha ngakhale mwini wa mpeniwo.
Mpeni wakuthwa konsekonse.
-Munthu wokonda kukometsa kuwiri, mthirakuwiri. Munthu
wotereyu amati akapita uku, amakatapa nkhani kumeneko
153