Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 151
Miyambi ya Patsokwe
ndi mafunso ndiye akusowa choyankha.
Mluzu wa agalu ndi umodzi.
-Munthu wanzeru sadikira kuti amve uthenga wakewake. Pa zo-
chitika zina monga maliro kapena msonkhano timafunika ku-
chita zinthu mofulumira komanso mogwirizana.
Mmene ndalimira ndi msana wanga sindingalephere kudyapo.
-Munthu amayenera kusangalala ndi ntchito imene wagwira ko-
manso zimene wazivutikira kuti azipeze.
Mnyanga sulemera mwini.
-Ana kapena abale ako ngakhale atakhala ovuta kapena olumala
timafunika tisatope nawo chifukwa amadalira ifeyo basi.
Mnzako akakuchenjeretsa pogona, iwe umuchenjerere podzu-
ka.
-Ngati mnzako ali ndi luso linalake lomwe iwe ulibe, uyenera
kulimbikira zimene umachita bwino kuposa iyeyo.
Mnzako akakutema mphini kumbuyo, iwenso umuteme kum-
buyo.
-Mnzathu akatithandiza, ndi bwino kudzamuthandizanso
akadzavutika m’malo mobweza chipongwe.
Mnzako akakuti konzu, nawe umam’ti konzu.
-Mnzako akukuchitira zabwino nawenso ndi bwino kumuchitira
zabwino.
Mnzako akapsa ndevu m’zimire.
-Tizithandiza anzathu akakhala pamavuto chifukwa tsiku lina
tidzawafuna.
Mnzako akapsa ndevu mzimitse, mawa adzazimitsa zako.
-Mnzako akakhala pamavuto muthandize chifukwa mawa akho-
za kudzakuthandiza iweyo.
150