Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 132
Miyambi ya Patsokwe
zokongola kwenikweni.
Maso apatali mkango ukunga nyani.
-Chinthu chikakhala patali sichidziwika bwino. Tiyenera ku-
chiyandikira kuti tichione bwinobwino.
Maso apatali, phiri limakhala losalala, ukaliyandikira si zig-
wembe zake.
-Zinthu zina zimangokongola m’maonekedwe pomwe si zokon-
gola kwenikweni.
Maso ndi madiwa.
-Nthawi zambiri timatengeka ndi zinthu zoipa kapena zabwino
chifukwa choti taziona. Mwachitsanzo, ena amachita chiwerew-
ere chifukwa choti aonera zolaula.
Maso ndi msampha.
-Nthawi zambiri timatengeka ndi zinthu zoipa kapena zabwino
chifukwa choti taziona. Mwachitsanzo, ena amachita chiwerew-
ere chifukwa choti aonera zolaula.
Maso ngati kapachike.
-Umbombo si khalidwe labwino. Mawu okuluwika otanthauza
kuti akasunge chakudyacho mpaka alendo atapita.
Maso saadya.
-Kuona chinthu sindiye kuti uchitenga kapena uchiwononga.
Mawuwa amanenedwa munthu akamanena kuti akungofuna
kuona sikuti atenga chinthucho.
Maso sakhuta.
-Maso sakhutitsidwa ndi zimene umaona. Tisalole kuti ati-
pusitse.
Maso sakhutsa n’kupenya.
-Kumangoyang’ana zinazake sikungathandize kuti chitheke ko-
ma kugwira ntchito. Mawuwa anganenedwenso kwa munthu
131