Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 114
Miyambi ya Patsokwe
Kwa eni uyenda umayeteka.
-Kuchilendo sukhala ndi ufulu wochita kapena kuyankhula chil-
ichonse chimene ukufuna.
Kwa eni, kapitolosi umaika m’kamwa.
-Munthu ukakhala kwa eni umakhala opanda ufulu wochika
kapena kuyankhula chilichonse chimene ukufuna. Tiyenera ku-
khala odzichepetsa tikhala kwa eni. Kapitolosi ndi ndevu za
pamlomo.
Kwafa galu kulibe mbiri.
-Munthu wosadziwika akalakwa, choipa chake sichidziwika
kwambiri. Munthu wodziwika akalakwa, mbiri imapita patali.
Kwagwa chauta.
-Mawuwa amanenedwa kukachitika mliri womwe wapulula an-
thu ambiri kapena kukachitika maliro.
Kwagwera mtengo wanthambi sikusowa.
-Anthu otchuka akalakwa mbiri imafala kwambiri, koma osatch-
uka nkhani yake sidziwika kwenikweni.
Kwakuchera uname.
-Pali anthu ena omwe kukangocha ntchito imakhala kunena
miseche. Ukanena zabodza suchedwa kugwidwa.
Kwakula kometa, waperewera kundwe (pawudala).
-Pogwira ntchito pamafunika anthu okwanira. Mawuwa
amanenedwa ikakhala kuti ntchito ndi yambiri koma anthu ndi
ochepa.
Kwalusa n’kulinga wina atajiwa.
-Timachenjera kwambiri pavuto ngati wina zamuonekera.
Kwanu n’kwanu, m’nthengo mudalaka njoka.
-Osamanyoza kwanu chifukwa zinthu zikakuvuta umabwerera
kwanu.
113