Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 98

Matigari “Ndine wogwira ntchito,” anaitokosa motero. “Ndakhala ndikugwira ntchito pafakitale imene ija kwa zaka zosawerenge- ka ndipo zimene Matigari wanena ndi choonadi chokhachokha. Ndakhala ndikugwira ntchito mokhulupirika kwa moyo wanga wonse. Koma tangoonani mmene mashini ayamwira mphamvu zanga. Mashini asungunula minofu yanga yonse moti ndan- gotsala mafupa okhaokha. N’chifukwa chaketu ndikungooneka ngati nzukwa. Thupi langa likungoyoyoka ngakhale ndiku- madzilimbitsabe mtima kuti zidzayenda. Ndakhala ndikuziuza kuti: ‘Munthu wolimbikira savutikiratu; munthu wopirira ama- pambana; anamwa tiyi adzamwanso, bola osataya masipuni.’ Koma kodi ndidzatsala ndi chiyani ndikadzapuma pantchito? Adzangondipatsa nsalu pothokoza chintchito chonse chomwe ndakhala ndikugwira mokhulupirika kwa zaka zonsezi. Zoona kugwira ntchito zaka zonsezi koma osalandira penshoni. Kodi mukudziwa? Ndakhala zaka zonsezi ndisakunyanyala nawo ntchito kapena kuchita ziwonetsero zosonyeza kusagwirizana ndi kuchepa kwa malipiro. Ndinkadziuza kuti: ‘Ndikachita na- wo zimenezi n’kundichotsa ntchito, ndipeza kuti ndalama zo- gulira chakudya cha ana anga?’ Koma taonani tsopano. Ndamangidwatu popanda chifukwa n’chimodzi chomwe. Ndiye mwina mukufunsa kuti ndiye ndabwereranji kuno? Dikirani ndikuuzeni.” “Masanawa, ndimayenda mphepete mwa nsewu n’kumapita kunyumba kwanga. Ndimadziuza kuti: ‘Bola ndisiyire kunyan- yala ntchitoku anthu ochenjera mopusawa, ndiwasiye akumvet- sera anthu ankamwa mwakukha uchi ngati Ngaruro wa Kiriro.’ Munthu wina wamsinkhu wangawu anaima n’kundifunsa kuti: ‘Kodi mwamva zimene zachitika?’ ‘Kwachitika chiyani? Mesa anthu akunyanyala ntchito chifukwa choti malipiro achepa?’ 97