Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 95

Matigari “Ndinkakhala pafamu yomwe Mtsamunda Williams anaba. Ndinasosa nthaka, ndinalima munda, ndinadzala mbewu ko- manso ndinasamalira mbewu. Koma kodi chinachitika n’chi- yani ndi mbewu zomwe ndinakolola? Zonse zinapita kunk- hokwe za Mtsamunda Williams ndipo ine munthu yemwe ndi- naswa mphanje, ndinasiyidwa kuti ndizidya zokunkha. Mtsamunda Williams ankayasamula chifukwa chokhuta. Pom- we ine ndinkayasamula chifukwa cha njala.” “Si zokhazoyi. Ndinamanga fakitale ya khofi komanso ya tiyi. Mwawadziwa mafakitale opanga zakudya kuchokera ku zipatso aja? Ndi ine ndinamanga mafakitale amene aja ndi en- anso ambirimbiri. Ndinamanga zonsezi ndi manja angawa, ndi zala khumi mukuzionazi. Koma kodi ndi ndani amene anatenga mapulofiti onse? Mtsamunda Williams. Nanga bwanji ineyo? Anangondiponyera kakhodo koti ndikagulire chingambwe basi. Kenako nthawi yoti ndilandire malipiro anga ochepa inakwana. Koma kodi mukudziwa amene ndinkakuma- na nawo pageti? Anali otolera misonkho a Mtsamunda Wil- liams. Ndikangolephera kupereka msonkho ankandikwidzinga ndi unyolo n’kukanditsekera kundende. Ndikalipira ndinkatsa- la ndi ndalama yokhala ngati yopatsa mwana kuti akadyere kusukulu.” “Musanganize kuti zinkachitika ndi zokhazi basi! Ndi man- ja angawa ndinamanga nyumba. Koma womangane ndinkago- na pakhonde, mwinanso kumachita kupemphetsa malo oti ndigone. Nthawi yonseyi Mtsamunda Williams ankakhala m’nyumba ndinamanga ine ija. Tandiuzeni, kodi ndi chilunga- mo kuti telala aziyenda buno bwamuswe, womanga kumagona pamtetete komanso wolima kumagona ndi njala, ndi chilunga- mo chimenecho?” 94