Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 92
Matigari
Palibenso chikondi chotere,
pakati pa amayi ndi ana.
Choti nyemba ikagwera pansi,
amagawana n'kudya limodzi.
Tiyeni tonse tigawane nyemba imodziyi, komanso kamowa
kali m'botoloka.”
Pali chinachake chomwe chinali m'mawu a Matigari chomwe
chinachititsa onse kuyamba kumumvetsera mwatcheru. Mawu
akewo anali achifundo, komanso anali ndi mfundo zopatsa
chiyembekezo ndi chilimbikitso. Ena onse aja anangokhala duu
n’kumamvetsera. Mawu akewa anawakumbutsa zinthu zomwe
anali ataziiwala, zinawakumbutsa za maloto omwe anali nawo
kalekalero.
“Ndiye tiona bwanji mumdima ngati umenewu?” Uja anag-
widwa akungoyendayenda m'tauni uja anafunsa.
“Palibe amene amaphonya pakamwa pake!” Uja ankaim-
bidwa mlandu wopha munthu uja anatero.
“Nanga bwanji chakudya china chitagwera pankodzo,” uja
anagwidwa akufuna kuba kachikwama uja anatero.
“Mwinanso chikhoza kugwera pamasanzi,” wakuba nsima
uja anawonjezera.
“Basi, masanzi komanso mkodzowo ukhoza kungosanduka
supu wathu,” mwana wakuyunivesite uja ananena moseleula.
“Utisanzitsa iwe!” anagwidwa ndi mlandu woyendayenda
uja anatero moipidwa. “Sukudziwa kuti mitima ya enafe
sichedwa kuyamba kuyendayenda?”
“Komanso enafe mutithawitsira chilakolako choti tidye,”
anatero ankafuna kuba kachikwama uja.
91