Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 90
Matigari
Anthu ena amatha kukhalabe zitsiru ngakhale atamera ndevu.
Basitu, kumene apolisi anatulukira sindinakuone. Kenako ananditsira
unyolo pamlandu wochita zinthu zovutitsa.
Wina anali mphunzitsi yemwe anamangidwa pamlandu
wophunzitsa ziphunzitso za Marx komanso ziphunzitso zina
zachikomyunizimu kusukulu.
“Kodi mukudziwa chifukwa chimene akundiimbira mlandu-
wu? Ati chifukwa choti ndinanena kuti mfundo zimene mayiko
monga Soviet Union, China, Cuba komanso mayiko ena
achikomyunizimu amayendera ndi zimene Marx ndi Lenin an-
kaphunzitsa. Koma ndili ndi funso limodzi. Ngati nditalephera
kuphunzitsa ana zinthu zoona, ndiye ndiziwaphunzitsa chi-
yani?”
Munthu wachisanu ndi chiwiri anamangidwa chifukwa anali
ndi cholinga chotsomphola kachikwama kam'manja ka mayi
wina wochita bwino.
“Ndinaona mayi wina wotchena akuwerenga mulu wa ma
100 shilings ndipo mumtima mwanga ndinangoti: Ndalama izo
zimayenera kukhala zathu. Ofunika ndizitenge kuti ndimuthan-
dize kuzigwiritsa ntchito. Ndiye ndinayamba kumutsatira. Atan-
gotsala pang'ono kulowa mu Mercedes-Benz, ndi . . . nanga ndi-
kanadziwa bwanji kuti pafupi ndi ine panali wapolisi yemwe sa-
navale yunifomu? Basitu anandimbwandira pamlandu wakuba.”
Woledzera uja anamangidwa chifukwa chopezeka atamwa
mowa mopitirira muyeso.
“Kodi zimenezizi ndi zomveka?” anafunsa motero,
“Ndikapanda kumwa mowa ndiye ndizichita chiyani ndi moyo
wangawu?
Pofika pano, ndi Matigari komanso anthu ena wiri omwe
89