Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 88
Matigari
“Mukudziwa, nthawi zina zimene anthu oledzera amakamba
zimakhala ndi kanthu kenakake kanzeru!”
“N'chifukwa chake ena amati mowa ukhoza kuthandiza
munthu kuzindikira zinthu zozama. Oledzera akhoza
kutitsegula m’maso kuti tithe kuzindikira zinthu zofunika.”
“Zimenezo ndi zoona, chifukwa zimene woledzerayu
wanena ndi choonadi chenicheni. Dziko lathulidi ndi louma gwa
ngati konkireti ili pansiyi. Atsogoleri athu ali ndi mitima youma
ngati ya Farao. Mwinanso youma kuposa ya atsamunda aja. Iwo
samva kulira kwa anthu a m'dziko lawo.”
“Zimenezo ndi zoonadi, nanga mungandifotokozere
bwinobwino chifukwa chake apolisiwa andimanga lero?”
“Nanjinanji ine!”
Kenako onse anaiwala za mkodzo wa woledzera uja ndipo
anayamba kufotokozerana zimene zinachitika kuti amangidwe.
Mmene ankachezera zinkangokhala ngati akhala akudziwana
kwa zaka zambiri.
M'modzi mwa anthuwo anali mlimi. Anali atamangidwa
popezeka akugulitsa mkaka popanda chilolezo.
“Linalitu botolo limodzi lenileni! Pamene ndimachokera ko-
kagula makandulo kuti ndidzipita kunyumba ndinangowaona
atulukira, kenako ndinangozindikira anditsira unyolo amvekere:
'Tionetseni chikalata chokulolezani kugulitsa mkaka m'tauni
muno.'”
Wina anamangidwa ataba nsima pamalo ena ogulitsira
chakudya.
“Nanga ine ndikanatani mwana wamatumbo atavuta? Ndi-
nali nditatheratu ndi njala moti sindikanachitira mwina.”
87