Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 86

Matigari Gawo 13 Matigari anaponyedwa muselo ina yamdima momwe munali mutadzadza ndi mpweya wa anthu ena khumi omwe analongedzedwa m'menemo. Munkamvekanso fungo lonyansa kwambiri la masanzi a mowa, thukuta komanso magazi omwe anapakikapakika m'makoma a seloyo kwa zaka zambiri. Museloyo munalibe mpweya wabwino moti zinkangokhala nga- ti awatsekera m'botolo modzadza ndi fungo loipa. Matigari anayesetsa kuti achotse nseru yomwe inamugwira atangolowa museloyo. Museloyo munangoti zii kupatulapo mkonono wa chidakwa china chomwe chinali chitagona pamasanzi ake. Kenako m'modzi mwa anthu omwe anali museloyo anakuwa kuti: “Kodi ndi ndani amene akukodzayo?” “Ndi woledzera wagona apayu!” anthu angapo anayankha mogwirizana. Anthu omwe anali museloyo anayamba kudzipanikiza ku- khoma kuti mpope wamkodzo wa woledzerayo usawanyowetse, koma zinali zosatheka kusuntha chifukwa anali atagunda kale khoma. Ena anayamba kuyankhula momoipidwa kwambiri po- funa kusonyeza kuti zimene zikuchitikazo zikuwanyansa ndipo ena anayamba kulalata: “Posachedwapa anasanza! Pano ndi uyu akukodzayu!” “Kenako atinyerera ndithu!” “Tamutsinani adzuke!” “Tamukhomani!” “Iwe tadzuka, wewe pund a m ilia!”* m'modzi mwa anthuwo anamukhoma ndipo woledzerayo anadzuka. *Wewe punda milia! (Kiswahili): kutanthauza, “Mbuzi iwe!” 85