Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 80
Matigari
tinamutumiza kuti akachite maphunziro, tikumanena kuti mwa-
na wanzako ndi wako yemwe, ukachenjera manja umadya naye?
Tikumanyadira kuti tsogolo la dziko lathu lagona mwa mwana
ameneyu, mwana yemwe adzatimenyere nkhondo yolimbana
ndi atsamunda! Koma tikanadziwa tikanangokazinga ndithu!
Mbewu tinadzalayi ndi chitedze chenicheni."
"Tandimvetserani bwinobwino. Mzee, ndikufuna ndikupem-
pheni kuti muphunzire tanthauzo la mawu akuti ‘munthu.’ Dzi-
ko lathuli lakhala lili mumdima wandiweyani chifukwa cha um-
buli wa anthu athu omwe sadziwa tanthauzo la mawu ame-
newa. Anthu ake sadziwa kufunika kwa mawu akuti, ‘munthu,’
mosiyana ndi mawu akuti ‘chigulugulu.’ Azungu akutukuka
chifukwa amazindikira tanthauzo la mawu amenewo, choncho
amalemekeza ufulu wa m unthu, zimene zikutanthauza kuti
munthu aliyense ali ndi ufulu wochita zimene akufuna mosasa-
mala kanthu kuti ena amaziona bwanji. Chulukechuluketu ngwa
njuchi. Koma anthu akudanu mumachita zinthu ngati winawake
anakumangirirani banja, fuko, dziko komanso anthu amtundu
wanu pamsana. Munthu wina akamafuna kuchita zinthu zomwe
zingamuthandize kuti atukuke komanso apite patsogolo,
mumamugwira juzi n’kumamukokera m'mbuyo. Kodi mawu
akuti 'chigulu' amatanthauza chiyani? Mzee, ndikufuna
ndikuuzeni kuti nkhokwe yagulu imakhala yopanda kathu.
Nthawi zonse zinthu zagulu zimanyamulidwa m'chidebe
chopanda matako. Chifuyo cha aliyense chimafa ndi njala. Kodi
paja nyimbo ija imati chiyani? Yend a bw ino aise tio nana, ali-
yense ayendere yake. Sikuti thupi langa laphukira pansama pakopo ko-
manso sikuti pali amene wabereka mnzake! Bambo anga ankadziwa
zimenezi, n'chifukwa chake ananditumiza kusukulu. Iwo
anatseka mapirikaniro awo kuti asamve zomwe zitsiru zina
zinkanena, kuti tiyenera kugawana komanso kudyera limodzi
79