Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 73
Matigari
“Heyi, m zee,” * munthu wakuda uja anafuula motero. “Kodi
sukuona chikwangwanicho? Hak una njia.* Ha ha ha! . . . Kapena
sumatha kuwerenga? Komansotu imeneyo si njira yopita
kunyumba za ogwira ntchito.”
*Mzee (Kiswahili): Kutanthauza “Munthu wokalamba kapena kuti Madala.”
*Hakuna njia (Kiswahili): Kutanthauza “Palibe njira.”
Matigari anatembenuka, n’kuyang’ana munthu uja kwa kan-
thawi, kenako anamufunsa kuti:
“Kodi kumeneko n’kumene kuli makiyi?”
“Makiyi a chiyani?”
“Makiyi otsegulira m’nyumba.”
“Nyumba yake iti?”
“Iyiyi.”
“Ukufuna utani nawo makiyiwo?”
“Mukufunsatu chinyezi kubafa, kapena nditi fungo
m’chimbudzi! Moti simukudziwa kuti makiyi timatsegulira
chitseko? Ndikufuna ndikatsegulire chitseko cholowera
m’nyumbayi! Ndakhala ndili koyenda kwa nthawi yaitali ndiye
ndabwerako tsopano.”
“Ndiye ukuganiza kuti iyiyi ndi nyumba yogona alendo?”
Munthu wakuda uja anafunsa mwakachipongwepongwe ee.
“Bob, tabwera udzamve zimene mdalayu akunena, eti akuti nyumbayi
ndi yake!”*
*Kugonekedwa kwa mawuwa kukusonyeza kuti anthuwa akuyankhulana
Chingerezi osati Chigikuyu.
Munthu wakuda uja tsopano anatsika pahatchi ija atagwira
chingwe chokokera hatchiyo n’kumalowera kumene kunali
Matigari. Mnzake uja, yemwe anali adakali pahatchi anabweran-
so chapafupi. Matigari anali atagwira geti lolowera kumene
72