Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 67

Matigari Gawo 11 Pa nthawiyi n’kuti chithunzithunzi chitatalika chifukwa dzu- wa linali litatsika ndithu. Komabe, kunja kunkatenthabe kwam- biri. Udzu unali utafota ndipo nawonso masamba a mitengo ankaoneka kuti atoperatu kuwaulidwa ndi dzuwa. Mpweya womwe unali patsikulo unali wa bee, ndipo pamsewu waphula pankakhala ngati pamwamba pa uvuni yomwe yangowotched- wa kumene. Ukamauonera patali nsewuwo, unkachita kuoneka ukutulutsa m’bebe. Kupatulapo phokoso la galimoto zomwe zinkayenda mumsewuwo komanso kulira kwa mbalame m’mi- tengo, kunja kunangoti zii ngati kulibe anthu. Kunalibiretu mphepo. Sikunkamveka phokoso la masamba komanso m’makuka onse omwe anawadutsa, palibe khomo limene pa- nayanikidwa zovala. Posakhalitsa anakumana ndi malole atatu odzadza ndi asilikali komanso ma Land-Rover anayi a apolisi. Asilikaliwo anali atanyamula mifuti komanso zida zina zankhondo. Ko- manso wapolisi aliyense anali atanyamula chamboko, chishango komanso chovala chodzitetezera ku mpweya wokhetsa misozi. “Kodi akulowera kuti awa?” Anafunsa Matigari. “Akupita kufakitale,” anayankha Guthera. “Pajatu ogwira ntchito kufakitale ananena kuti ayamba kunyanyala ntchito kuyambira 2 koloko masana a lero.” “Ndiye akupita kukamenyana ndi ogwira ntchitowo kapena bwanji?” Matigari anafunsa. “Bamboyutu wakhala zaka zambiri m’tchire.” Guthera anad- ziuza mumtima mwake. “Akufunika kupita kaye kunyumba n’kukapha tulo komanso kutopa konse komwe wakhala akusungira zaka zomwe wakhala m’tchire. Ndi ndani m’dziko 66