Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 65
Matigari
yachipambano mumtima mwanga: Nyum ba ija nd i yanga
tsopano. Ndi ya ine komanso banja langa . . . N’chifukwa chaketu
ndikufunafuna anthu a m’banja langa, ana anga aamuna ndi
aakazi, azilamu komanso apongozi anga, azikazi anga . . .”
“Ngakhalenso azikazi anu? N’chifukwa chiyani munawasi-
ya?” Guthera anafunsa mokhala ngati akukayikira zoti mutu wa
Matigari umagwira. Iye ankadzifunsa kuti, “N’chifukwa chiyani
akuyankhula zopanda nzeruzi?”
“Nanga ndinakawasiya kuti mwana wanga? N’chifukwa
chaketu ndinatenga zida n’kuthawira kunkhalango komanso ku-
mapiri kuti ndikamenye nkhondo n’cholinga choti nawonso
akhale ndi nyumba. Koma pali vuto, kodi ndikawapeza kuti
tsopano? Ndiyambira pati kuwafunafuna?”
“Kodi munapita kuminda ya tiyi komanso khofi?” Guthera
anafunsa akuoneka kuti akuchita manyazi chifukwa chokayikira
kuti mutu wa Matigari umagwira. Iye anali atakumbukiranso
kuti Matigari ndi amene anamupulumutsa kuchokera m’kamwa
mwa galu wolusa uja.
“Zoona mpaka pano adakagwirabe ntchito ngati akapolo
m’minda ya tiyi?” anafunsa Matigari.
“Nanga mumafuna kuti azitani? Masiku ano palibe malo om-
we simungapeze azimayi akugwira ntchito kuti apeze kangache-
pe koti akagulire chakudya cha ana komanso azimuna awo,”
Guthera anatero, “Azimayi ambiri amagwira ntchito m’minda ya
tiyi, khofi komanso gonje. Ngati mukufuna kupeza azikazi anu,
koyambira kwabwino kungakhale kuminda imeneyi. Pitani
mukayambe ndi kupulumutsa amenewo, musadandaule za ife
chifukwa moyo wathu unatayika kalekale m’mabala muku-
waonawa.”
64