Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 52

Matigari Nthawi iliyonse imene Guthera ankadzuka kuti athawe, galuyo ankamulumphira, kwinaku akuuwa mochititsa mthumanzi ko- manso akubangula ngati wamva fungo la magazi. Anthu ena ankangoseka, ndipo zinkaoneka kuti zimene zikuchitikazo zinkawamaliza koopsa. Kenako nkodzo unayamba kuyenderera pamiyendo ya Guthera. Ankachita mantha kwambiri chifukwa ankaganiza kuti galuyo amukhadzulakhadzula basi. Matigari ataona izi mtima wake unamuwawa zedi. Ankango- khala ngati wina akumukolokosa pachilonda. Anayendetsa manja m'chiuno mwake ngati mmene ankachitira pa nthawi yonse yomwe ankalimbana ndi Mtsamunda Williams kumapiri kuja. Koma sanapezemo kalikonse. Iye analibe mfuti yake. Tsopano anakumbukira kuti anali atavala lamba wamtendere. Koma anali atanyangala ndi nkwiyo woopsa. Iye anadzifunsa kuti: “Ndi munthu wamtundu wanji yemwe amalephera kute- teza ana ake?” Komabe sikuti anangoutsekera mkwiyowo mumtima. Nthawi zonse ankadziuza kuti palibe chifukwa chokwiyira ndi zinthu ngati sukufuna kuchitapo kathu kuti uzisinthe. Kenako anauza gulu la anthu aja mokwiya kuti: “Kodi chikuchitika n'chiyani apa? Anthu akuluakulu ngati inu mungangoima pamenepopo muli ndevu pepeyaa, n'ku- maonerera mwana wanu akudyetsedwa matudzi ndi anthu oipa mitimawa? Zoona makosana nonsenu mungamagwedezere mitu n'kumavomereza kuti anthu ankhanza azizunza ana osalakwa? Ndi usiwa wam’maganizo wamtundu wanji womwe wakugwirani kuti muzingoonerera mtsikana wokongola ngati uyu akupondedwapondedwa ndi chilombo?” “N'chiyani chikukuseketsani pamenepa? N'chifukwa chiyani mumadziphimba ndi nsalu ya mantha, n'kulolera kuti mantha 51