Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 50
Matigari
“Kodi sukuona kuti ndine wamsinkhu wofanana ndi bambo
ako?” Matigari anauza Guthera pamene anapeza kampata ko-
yankhula. “Tachoka pamiyendo pangapa msanga!” ananena
zimenezi akumukankha.
Kenako Guthera anakhala pakati pa Matigari ndi Muriuki.
“Kodi mwakhala muli kuti bambo inu? Kodi mwachokera
kumwezi, m’mlengalenga kapena? Kapena mukungofuna muy-
erekedwe kaye? Taimani ndikuuzeni: Masiku anotu sitikusama-
la za aliyense. Kaya ndi bambo ako, mwana wako, kaya ndi
mchimwene wako kapena mchemwali wako, tilibe nazo ntchito.
Nkhani yofunika kwambiri ndi makobidi basi. Ngakhale mwa-
na ngati uyu ali apayu, ndikhoza kumuchengetera bwinobwino
mpaka kumuiwalitsa kwawo. Eti ukuganiza bwanji mchim-
wene? Anthu okhawo amene ndinalumbira kuti sindidzayereke-
za kuchita nawo uhule ndi apolisi. Kapena nanunso ndinu wap-
olisitu? Dzina lanu ndi ndani?”
Matigari asanayankhe, Guthera anayang’ana chakuzenera
ndipo anaona apolisi anali ndi galu aja. Anadzidzimuka kwam-
biri atawaona moti anangoti balamanthu n’kuimirira.
“Kalanga ine! Afisi awiri aja akubwera kuno . . . Sindikufuna
kuti zitsiru zimenezi zindipusitse. Musachoke bambo, mundidi-
kire pomwepa. Ndikubwera posachedwapa. Ndikabwera
mudzandigulira umodzi eti?”
Kenako Guthera anatuluka panja.
Matigari anagwira chibwano chake mokhumudwa kwambiri
akuganizira zimene zinachitikazo. Ankakhala ngati waikira mu-
tu wake jeke. Mutu wake womwe unayamba kumulemera.
Pachipumi pake panali patathethekanso mizere yatsinya la
ukalamba. Tsinyalo linakula kwambiri moti linkangokhala ngati
49