Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 34
Matigari
Gawo 7
“Nanga ndiwe ndani mwana wanga?” bamboyo anafunsa.
“Ndani, mukunena ineyo?” munthuyo anayankha motero.
“Dzina langa ndi Ngaruro wa Kiriro.”
“Ngaruro? Wa m’banja la Kiriro? Zikomo kwambiri. Tsiku
lina tizadziwana bwinobwino pa nthawi imene tidzasiye
kuponyana miyala. Kodi ndi kuti kumene tingapeze malo oti
tibisale dzuwa likuwirimali? Mukudziwa malo aliwonse abwino
komwe tingaguleko chakudya cha ine ndi . . . ”
“Muriuki. Dzina langa ndi Muriuki.”
“Inde, malo omwe ine ndi Muriuki tingaguleko chakudya?”
Kenako anamutembenukira n’kumufunsa kuti, “Kapena
ukufuna kubwerera kumudzi wanu?”
Muriuki anakayikira. Iye ankaona kuti bamboyo wavulala
kwambiri moti sankafuna kungomusiya yekha. Komanso nanga
akanamusiya bwanji atamva zoti akufuna kugula chakudya?
“Aa, kaya!” mwanayo anayankha. “Ngati nditabwerera,
mnyamata anandimenya uja akandimenyanso. Akhozanso
kukandilanda zinthu zanga. Amakonda kumenya anzake amene
uja. Komanso anyamata ena aja akandilanga chifukwa
chokutengani inuyo, munthu woti sindikumudziwa,
n’kukupititsani kumudzi wathu. Akhozanso kukandimenya
chifukwa chokulolani kuti mudutse malire olowera m’mudzi
wathu. Zingakhale bwino nditapanda kupitako kwa masiku
awiri kapena atatu kuti aiwale kaye za nkhaniyi.”
“Kodi nawenso umakhala m’mudzi wa ana uja?” Ngaruro
anafunsa.
“Inde, ndimakhala komweko,” mwanayo anayankha
motero.
33