Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 274

Matigari Gawo 21 Pansi pa mtengo wakachere paja, Muriuki anafukula zinthu zonse zomwe Matigari anakwirira. Iye anafukula pistole komanso lamba wazipolopolo uja. Ndiyeno anayamba kuwerenga zipolopolozo. Anatenga AK47 n’kudzaiyang’ana bwinobwino. Kenako anatulutsa chikanda- langa chija n’kuchiika pansi pambali pa mwendo wake. Lamba wazipolopoloyo anamukoleka pakhosi pake modutsa paphewa lake lakumanzere. Anakolekanso chingwe cha chimake cha chikandalanga chija paphewa lake lamanja ndipo chikanda- langacho chinkalendewera chamunkhwapa mwake. Kenako anatola mfuti ya AK47 ija n’kuikoleka paphewa. Ndiyeno anaima kaye pang’ono pansi pamtengo wakachere uja. Posakhalitsa anamva kulira kwa mapazi chapafupi. Mtima wake unanyamuka. Koma inali hatchi yopanda munthu ndipo hatchiyo inathamanga n’kumudutsa. Hatchiyo inaima pang’ono n’kuyamba kumuyang’ana ngati ikumudziwa. Kenako inalowa m’ziyangoyango n’kuzimiririka. Muriuki ankangoyang’ana mvula yomwe inkakhuthuka ija. Iye anaima n’kumayang’ana chakumene kunali mtsinje kuja. Anayang’ana kutsidya lina la mtsinjewo komanso kuchigwa chomwe chinali kutsogolo kwake ndiponso mapiri omwe anali chapatali. Chapatali kwambiri, anamva kulira kwa sailini yomwe n’kutheka inkaitana ogwira ntchito kuti akayambepo. Iye anakumbukira tsiku lomwe ogwira ntchito anachita sitiraka. Ndipo mwadzidzidzi anayamba kumva mawu cha- pansipansi. Mawuwo anali a ogwira ntchito, alimi komanso ophunzira pasukulu yaukachenjede komanso anthu ena 273