Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 251
Matigari
Maso awo anaphana. Anali Giceru, kazitape uja, munthu
yemwe uja anamangidwa naye limodzi m'ndende.
Matigari anamuona akuyankhula ndi munthu wina wog-
wira ntchito pagalaja. Ndipo anthu awiri onsewo anayamba
kuyenda molowera kumene kunali galimoto kuja.
Matigari anayamba kudya mapulani. Panalibenso galimoto
ina pamalowa. Choncho njira yokhayo imene anthuwa akanalu-
mikizana ndi anthu inali kudzera palamya basi. Kenako ana-
manga mfundo imodzi. Anakwera m'galimoto ija, kuliza injini
n'kuyamba kuyendetsa.
Iye ankadziuza kuti, ‘Kazitapeyu akhoza kuchita chilichonse
chimene akufuna. Munthu amafa kamodzi basi!’
Posakhalitsa Giceru anaimbadi foni.
250