Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 249

Matigari Gawo 18 Matigari anayenda mofulumira kulowera kumene kunali chitsime chomwetsera mafuta cha Esso kuja, komwe anaimikako galimoto ya Mercedes-Benz. Mwadzidzidzi, anaima kaye. Kupatulapo galimoto yandu- na ija, pamalowa panalibenso galimoto ina yamtundu wa Mer- cedes-Benz ndipo panalibenso ngakhale magalimoto ami- tundu ina. Iye ankadzifunsa kuti, kodi kapena anditchera msampha? Anayang'ana malo ozungulira akuganiza kuti n'kutheka kuti penapake pali apolisi. Koma sanawone wapoli- si aliyense. Kenako anayamba kulowera kumene kunali chitsime chomwetsera mafuta kuja ndipo anakagula mafuta m'chigubu. Pa nthawi yonseyi, ankayang'ana mochenjera kwambiri kuti aone chimene chikuchitika. Mkati mwa ofesi yomwe inali pamalo ogulitsira mafutawo munali munthu yemwe ankasuta fodya. Matigari ankalephera kuona nkhope ya munthuyo bwinobwino. “Kodi galimoto zonse zija zalowera kuti?” Matigari ana- funsa munthu ankagulitsa mafuta uja. “Kodi simunamve?” “Kumva zotani?” “Dziko lonsetu lapita kunyumba kwa Boy.” “Kukuchitika chiyani? Kuli phwando kapena?” “Kodi mukunenetsa kuti simunamve zankhani imeneyi?” “Nkhani yake iti?” 248