Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 244

Matigari "Yesu Khristu? Ambuye yemwe adzabweretse Yerusalemu watsopano padziko lapansi pano?" wina anawonjezera. Matigari anakaikira kwa kanthawi. Kenako anayang'ana ana aja mowamvera chisoni. Ndiyeno anaponya maso ake chakutsogolo n'kumayang'ana ziphapha za magalimoto zija. "Ayi," Matigari anayankha. "Mulungu amene analo- seredwayo ali mwa inuyo, mwa ine komanso mwa anthu ena on- se. Iye wakhala ali mwa ife kuchokera pachiyambi pa chilengedwe. Olamulira opondereza akhala akufuna kupha Mulungu ameneyo mwa ife. Koma tsiku lina Mulungu ameneyo adzauka kwa akufa. Tsiku lina Mulungu ameneyo adzabwera n'kudzatipulumutsa tonse amene timamukhulupirira. Ndikunenazi sintchetera ayi." "Iye adzabwera patsiku limene otsatira ake adzathe kuima pamodzi popanda kuyang'ana fuko, mtundu kapena khungu ko- manso pamene onse adzagwirizana kuchita chimodzi. Khama lathu linatulutsa chuma chonse chili m'dziko muno. Choncho kuyambira lero tikukana kumagona pamtetete n'kumakupu- lidwa ndi mphepo. Tikukana kumayenda titavala masanza ko- manso kumagona nayo njala. Dzikoli likufunika libwerere kwa eni ake. Nthaka ibwerere kwa mlimi, mafakitale kwa ogwira ntchito . . . Koma Mulungu ameneyo amakhala kwambiri mwa inu ana a m’dziko muno. Ndiye ngati mutalola kuti dzikoli lipite kwa olamulira ankhanza komanso zidole zawo zomwe zim- awateteza, ndiye kuti mukupha nokha Mulungu ali mwa inuyo. N'chimodzimodzi kuchititsa kuti asaukitsidwe. Mulungu ameneyo adzabweranso kokha ngati mutamulola kuti abwere." Ana aja anayamba kuyang'anizana modabwa. Mawu a Matig- ari ankasinthasintha, koma zimene ananenazo zinawagwira mti- ma. 243