Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 236

Matigari chopuma, kenako n'kuyamba kuuluka ngati ndege kapena kuthamanga ngati hatchi. Iyeyo ankadziona ali pachiwongole- ro n’kumayendetsa. Naye Matigari ankaphika mapulani a mmene angapitire kukatenga zida zake kuti akatengenso nyumba yake. Mawu amene ankayendayenda m’mutu mwake anali akuti, ‘Mbewu imodzi ikalephera kumera sizichititsa mli- mi kuti asiye kudzala.’ Guthera nayenso sanasiye kuganizira za mzimayi uja. Iye ankamumvera chisoni kwambiri. Ankadzi- uza kuti, ‘Azimayife ndiye tili pamavuto aakulu! Kulikonse kumene tingalowere timakumana nazo zokhoma! Mzimayi uja akapita kwawo, mwamuna wake akamuthibula, ndipo akamu- funsa kuti anapezeka bwanji ndi mwamuna ali mbulanda m’chipululu. Nayenso bwenzi lakelolo likapita kwawo, likati- dzimula mkazi wake chifukwa wafunsa zoti amatani ndi mzi- mayi awiriwiri m’chipululu. Kenako Matigari anatsegula wailesi. M'galimotomo mu- nayamba kumveka nyimbo zapansipansi ndipo kenako inafika nthawi ya nkhani. . . . Boma la USA lakana pempho la boma la Soviet Union kuti padzikoli pachotsedwe zida zonse zanyukiliya* . . . Boma la USA lag- aniza zoyamba kusunga zida m'mlengalenga . . . Boma la USA ko- manso Soviet Union layamba kutumiza anthu enanso kuti apite kum- wezi . . . *Zimenezi zinalembedwa mu 1983, patadutsa zaka zingapo pambuyo pa msonkhano wa ku Reykjavik. "Anthu ake amangokhalira kulengeza nkhani zokhudza dziko la USA komanso Soviet Union! Amangobwereza nkhani zomwezomwezo mpaka zifike potinyansa. Kaya siz- imawatopetsa?" Anatero Guthera. 235