Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 232
Matigari
"Inde ndinabwerapo, kambirimbiri."
"Ine kano n'koyamba," anatero Muriuki.
Atafika kudera lomwe kunali makampani, Guthera anati:
"Kano ndi koyamba kufika mbali ino ya tauni." Anapitirizabe
kuyang'ana panja kudzera pawindo, ndipo ankawerenga
mayina a zikwangwani zomwe zinali m'mbali mwa nsewu.
"General Motors . . . Firestone . . . Coca-Cola . . . IBM . . . Un-
iliver Products . . . Madhvani Products . . . Del Monte . . . BAT . .
. Union Carbide . . . Mitsubishi Products . . . African Cycle
Mart . . ." Kenako anatopa n'kuwerenga zikwangwanizo ndipo
anayamba kuganizira za mzimayi uja. Ankadzifunsa kuti, ‘Kodi
mayi amene uja ndinamuona kuti?’
Kenako anadutsa nyumba zina za ogwira ntchito. Nyumba
zimenezi zinali zazing'ono kwambiri ngati zimbudzi moti
ukamazionera patali zinkangooneka ngati zinyalala. Zinali
zovuta kukhulupirira kuti munthu wabanja lake angakhale
m’kanyumba kakang’ono ngati kameneko. Kenako anayamba
kudutsa mafamu. Mipanda yomwe inazungulira mafamuwa in-
ali yooneka kuti inamangidwa kale kwambiri moti inali yakuda
bii. Ndipo kumpanda kwake kunkaoneka kuti kunalibe
chomera ngakhale chimodzi. Anthu oyenda pansi, mabasi, gal-
imoto zing'onozing'ono, anjinga komanso ngolo zingapo zinka-
kanganirana kuyenda munsewuwo.
Kenako anafika kudera limene kunkakhala olemera ndipo
Muriuki anayamba kuganiza kuti nyumba zimene ankaona ku-
meneku ndi zomwe anaziona m'magazini ya Natio nal Geo -
graphic yomwe anaitola m' bini ina. Anang' amba zithunzi za nyumba-
zo n'kuzimata m'nyumba yake ija ya Mercedes-Benz.
231